Ndipo Davide ananena ndi Abisai ndi anyamata ake onse, Onani, mwana wanga wotuluka m'matumbo anga, alikufuna moyo wanga; koposa kotani nanga Mbenjamini uyu? Mlekeni, atukwane, pakuti Yehova anamuuza.
Mateyu 10:21 - Buku Lopatulika Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuimfa, ndi atate mwana wake: ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuimfa, ndi atate mwana wake: ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Mbale azidzapereka mbale wake kuti aphedwe, bambo azidzapereka mwana wake. Ana adzaukira makolo ao, mpaka kuŵaphetsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe ndi abambo mwana wawo: ndipo ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe. |
Ndipo Davide ananena ndi Abisai ndi anyamata ake onse, Onani, mwana wanga wotuluka m'matumbo anga, alikufuna moyo wanga; koposa kotani nanga Mbenjamini uyu? Mlekeni, atukwane, pakuti Yehova anamuuza.
mabwenzi anga enieni onse anyansidwa nane; ndi onse ndakondana nao asandulika adani anga.
Ndipo ndidzapikisanitsa Aejipito; ndipo adzamenyana wina ndi mbale wake, ndi wina ndi mnansi wake; mzinda kumenyana ndi mzinda, ndi ufumu kumenyana ndi ufumu.
Ndipo kudzachitika, akaneneranso wina, atate wake ndi mai wake ombala adzanena naye, Sudzakhala ndi moyo, pakuti unena bodza m'dzina la Yehova; ndipo atate wake ndi mai wake ombala adzamgwaza ponenera iye.
Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mnzake, nadzadana wina ndi mnzake.