Ndipo tsopano muka, ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi kukuphunzitsa chomwe ukalankhule.
Mateyu 10:19 - Buku Lopatulika Koma pamene paliponse angakuperekeni inu, musamadera nkhawa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene chiyani; pakuti chimene mudzachilankhula, chidzapatsidwa kwa inu nthawi yomweyo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma pamene paliponse angakuperekeni inu, musamadera nkhawa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene chiyani; pakuti chimene mudzachilankhula, chidzapatsidwa kwa inu nthawi yomweyo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akadzakutengerani ku milandu, musadzade nkhaŵa nkumanena kuti, ‘Kodi tikakambe bwanji?’ Kapena kuti, ‘Kodi tikanene chiyani?’ Mudzapatsidwa pa nthaŵi imeneyo mau oti munene. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma pamene akumangani, inu musadandaule kuti mukanena bwanji kapena mukanena chiyani. Mudzapatsidwa pa nthawi imeneyo zoti munene, |
Ndipo tsopano muka, ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi kukuphunzitsa chomwe ukalankhule.
Ndipo ukalankhule naye, ndi kumpangira mau; ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi m'kamwa mwake, ndipo ndidzakuphunzitsani inu chimene mukachite.
Koma Yehova anati kwa ine, Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena chonse chimene ndidzakuuza.
Ndipo Yehova anatulutsa dzanja lake, nakhudza pakamwa panga; nati Yehova kwa ine, Taona ndaika mau anga m'kamwa mwako;
ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja.
Chifukwa chake ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala?
Chifukwa chake musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? Kapena, Tidzamwa chiyani? Kapena, Tidzavala chiyani?
Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.
Ndipo pamene paliponse adzamuka nanu kumlandu wa m'sunagoge ndi kwa akulu, ndi aulamuliro, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mau otani, kapena mukanena chiyani;
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.
Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.
Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.