Mateyu 10:12 - Buku Lopatulika Ndipo polowa m'nyumba muwalonjere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo polowa m'nyumba muwalonjere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Poloŵa m'nyumba, muzikanena kuti, ‘Mtendere ukhale ndi inu’. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene mulowa mʼnyumba mupereke moni. |
Chifukwa cha abale anga ndi mabwenzi anga, ndidzanena tsopano, Mukhale mtendere mwa inu.
Ndipo iwowa, ngakhale akamva kapena akaleka kumva, (pakuti ndiwo nyumba yopanduka,) koma adzadziwa kuti panali mneneri pakati pao.
Ndipo m'mzinda uliwonse, kapena m'mudzi, mukalowamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo; ndipo bakhalani komweko kufikira mutulukamo.
Ndipo ngati nyumbayo ili yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siili yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu.
Mau amene anatumiza kwa ana a Israele, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa Yesu Khristu (ndiye Ambuye wa onse)
Chifukwa chake tili atumiki m'malo mwa Khristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m'malo mwa Khristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.
ndipo muzitero kwa wodalayo, Mtendere ukhale pa inu, mtendere ukhalenso pa nyumba yanu, ndi mtendere ukhale pa zonse muli nazo.