Masalimo 98:4 - Buku Lopatulika Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi; kuwitsani ndi kufuulira mokondwera; inde, imbirani zomlemekeza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi; kuwitsani ndi kufuulira mokondwera; inde, imbirani zomlemekeza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Fuulirani Chauta ndi chimwemwe, inu dziko lonse lapansi. Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Fuwulani mwachimwemwe kwa Yehova, dziko lonse lapansi, muyimbireni nyimbo mofuwula ndi mokondwera. |
Anthu akondwere, nafuule mokondwera; pakuti mudzaweruza anthu molunjika, ndipo mudzalangiza anthu padziko lapansi.
Ndiponso ndidzakuyamikani ndi chisakasa, kubukitsa choonadi chanu, Mulungu wanga; ndidzakuimbirani nyimbo ndi zeze, ndinu Woyerayo wa Israele.
Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.
Chipululu ndi mizinda yake ikweze mau ao, midzi imene Kedara akhalamo; okhala mu Sela aimbe, akuwe kuchokera pamwamba pa mapiri.
Imbani m'mwamba inu, pakuti Yehova wachichita icho; kuwani inu, mbali za pansi padziko; imbani mapiri inu; nkhalango iwe, ndi mitengo yonse m'menemo; chifukwa kuti Yehova wapulumutsa Yakobo, ndipo adzadzilemekezetsa yekha mwa Israele.
mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.
Imba, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula, Israele; kondwera nusekerere ndi mtima wonse, mwana wamkazi wa Yerusalemu.
Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana mu Kumwambamwamba!
Zitatha izi ndinamva ngati mau aakulu a khamu lalikulu mu Mwamba, lili kunena, Aleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu;
Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, ndi kunena, Aleluya; pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.