Yehova, palibe wina wonga inu, palibenso Mulungu wina koma Inu; monga mwa zonse tazimva m'makutu mwathu.
Masalimo 97:9 - Buku Lopatulika Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi, ndinu wokwezeka kwakukulu pamwamba pa milungu ina yonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba pa dziko lonse lapansi, ndinu wokwezeka kwakukulu pamwamba pa milungu yonse ina. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti Inu Chauta ndinu Wopambanazonse, wolamulira dziko lonse lapansi. Ndinu amphamvu kupambana milungu yonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti Inu Yehova ndi Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi; ndinu wokwezeka kupambana milungu yonse. |
Yehova, palibe wina wonga inu, palibenso Mulungu wina koma Inu; monga mwa zonse tazimva m'makutu mwathu.
Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi.
Pakuti, taonani, adani anu, Yehova, pakuti, taonani, adani anu adzatayika; ochita zopanda pake onse adzamwazika.
Pakuti Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse.
Tsopano ndidziwa kuti Yehova ali wamkulu ndi milungu yonse, pakuti momwe anadzikuza okha momwemo anawaposa.
Yehova wakwezedwa; pakuti akhala kumwamba; Iye wadzaza Ziyoni ndi chiweruzo ndi chilungamo.
Koma Yehova ndiye Mulungu woona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya; pa mkwiyo wake dziko lapansi lidzanthunthumira, ndi amitundu sangapirire ukali wake.
pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina lililonse lotchedwa, si m'nyengo ino ya pansi pano yokha, komanso mwa iyo ikudza;