Akumveketsa pansi pa thambo ponse, nang'anipitsa mphezi yake ku malekezero a dziko lapansi.
Masalimo 97:4 - Buku Lopatulika Mphezi zake zinaunikira dziko lokhalamo anthu; dziko lapansi linaona nilinagwedezeka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mphezi zake zinaunikira dziko lokhalamo anthu; dziko lapansi linaona nilinagwedezeka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zing'aning'ani zake zimaŵalitsa dziko lonse lapansi, dziko lonse limapenya nkugwedezeka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zingʼaningʼani zake zimawalitsa dziko lonse; dziko lapansi limaona ndipo limanjenjemera. |
Akumveketsa pansi pa thambo ponse, nang'anipitsa mphezi yake ku malekezero a dziko lapansi.
Liu la bingu lanu linatengezanatengezana; mphezi zinaunikira ponse pali anthu; dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.
Gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa, njenjemerani pamaso pake, inu dziko lonse lapansi.
Koma Yehova ndiye Mulungu woona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya; pa mkwiyo wake dziko lapansi lidzanthunthumira, ndi amitundu sangapirire ukali wake.
Ndipo anatsegulidwa Kachisi wa Mulungu amene ali mu Mwamba; ndipo linaoneka likasa la chipangano chake, mu Kachisi mwake, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi chivomezi, ndi matalala aakulu.
Ndipo ndinaona mutatseguka mu Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi Iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nachita nkhondo molungama.