Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?
Masalimo 97:2 - Buku Lopatulika Pomzinga pali mitambo ndi mdima; chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsa mpando wake wachifumu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomzinga pali mitambo ndi mdima; chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsa mpando wachifumu wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mitambo ndi mdima waukulu zamzinga Chauta. Amalamulira molungama, mu ufumu wake mulibe tsankho. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mitambo ndi mdima waukulu zamuzungulira; chilungamo ndi kuweruza molungama ndiwo maziko a mpando wake waufumu. |
Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?
Chilungamo ndi chiweruzo ndiwo maziko a mpando wanu wachifumu; chifundo ndi choonadi zitsogolera pankhope panu.
Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda chiweruzo; Inu mukhazikitsa zolunjika, muchita chiweruzo ndi chilungamo mu Yakobo.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndikudza kwa iwe mu mtambo wakuda bii, kuti anthu amve pamene ndilankhula ndi iwe, ndi kuti akuvomereze nthawi zonse. Pakuti Mose adauza Yehova mau a anthuwo.
Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wa mphamvu yaikulu; ndi wosamasula ndithu wopalamula; njira ya Yehova ili m'kamvulumvulu ndi mumkuntho; ndipo mitambo ndiyo fumbi la mapazi ake.
Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!