Masalimo 97:12 - Buku Lopatulika Kondwerani mwa Yehova, olungama inu; ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kondwerani mwa Yehova, olungama inu; ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu ndi anthu a Chauta, kondwerani mwa iye, ndipo mumthokoze potchula dzina lake loyera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kondwerani mwa Yehova Inu olungama ndipo tamandani dzina lake loyera. |
Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.
Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima; ndipo fuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima.
Mulungu walankhula m'chiyero chake; ndidzakondwerera, ndidzagawa Sekemu, ndidzayesa muyeso chigwa cha Sukoti.
Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma Iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa chiyero chake.