Masalimo 96:5 - Buku Lopatulika Pakuti milungu yonse ya mitundu ya anthu ndiyo mafano, koma Yehova analenga zakumwamba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti milungu yonse ya mitundu ya anthu ndiyo mafano, koma Yehova analenga zakumwamba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja milungu yonse ya mitundu ina ya anthu ndi mafano chabe. Koma Chauta ndiye adalenga zakumwamba. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano, koma Yehova analenga mayiko akumwamba. |
Taona, iwo onse, ntchito zao zikhala zopanda pake ndi zachabe; mafano ao osungunula ndiwo mphepo ndi masokonezo.
Atero Mulungu Yehova, Iye amene analenga thambo, nalifutukula, nayala ponse dziko lapansi, ndi chimene chituluka m'menemo, Iye amene amapatsa anthu a m'menemo mpweya, ndi mzimu kwa iwo amene ayenda m'menemo;
Ndipo muona ndi kumva, kuti si pa Efeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, Paulo uyu akopa ndi kutembenutsa anthu ambiri, ndi kuti, Si milungu iyi imene ipangidwa ndi manja:
Tsono kunena za kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano, tidziwa kuti fano silili kanthu padziko lapansi, ndi kuti palibe Mulungu koma mmodzi.