Mlemekezeni chifukwa cha ntchito zake zolimba; mlemekezeni monga mwa ukulu wake waunjinji.
Masalimo 96:3 - Buku Lopatulika Fotokozerani ulemerero wake mwa amitundu; zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Fotokozerani ulemerero wake mwa amitundu; zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Lengezani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse, simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m'maiko onse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Lengezani ulemerero wake pakati pa mayiko, ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu. |
Mlemekezeni chifukwa cha ntchito zake zolimba; mlemekezeni monga mwa ukulu wake waunjinji.
Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Yehova, ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.
inde, ati, Chili chinthu chopepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israele; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale chipulumutso changa mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
Ndipo amitundu ambiri adzamuka, nadzati, Tiyeni, tikwere kuphiri la Yehova, ndi kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti Iye atiphunzitse njira zake, ndipo tidzayenda m'mabande ake; pakuti ku Ziyoni kudzatuluka chilamulo, ndi ku Yerusalemu mau a Yehova.
Ndipo ndidzaononga magaleta kuwachotsa mu Efuremu, ndi akavalo kuwachotsa mu Yerusalemu; ndi uta wa nkhondo udzaonongeka; ndipo adzanena zamtendere kwa amitundu; ndi ufumu wake udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko.
Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:
ndi kuti kulalikidwe m'dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kwa mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu.