Aleluya, Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake.
Masalimo 96:1 - Buku Lopatulika Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano; muimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano; muimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Imbirani Chauta nyimbo yatsopano! Imbirani Chauta, anthu a m'dziko lonse lapansi! Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Imbirani Yehova nyimbo yatsopano; Imbirani Yehova dziko lonse lapansi. |
Aleluya, Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake.
Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano; popeza anachita zodabwitsa: Dzanja lake lamanja, mkono wake woyera, zinamchitira chipulumutso.
ndipo aimba ngati nyimbo yatsopano kumpando wachifumu, ndi pamaso pa zamoyo zinai, ndi akulu; ndipo palibe munthu anakhoza kuphunzira nyimboyi, koma zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, ogulidwa kuchokera kudziko.
Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,