Yehova ali mu Kachisi wake woyera, Yehova, mpando wachifumu wake uli mu Mwamba; apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.
Masalimo 94:9 - Buku Lopatulika Kodi Iye wakupanga khutu ngwosamva? Kodi Iye wakuumba diso ngwosapenya? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi Iye wakupanga khutu ngwosamva? Kodi Iye wakuumba diso ngwosapenya? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi amene adalenga makutu, sangathe kumva? Kodi amene adapanga maso, sangathe kupenya? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi Iye amene anapanga khutu sangathe kumva? Kodi Iye amene anapanga diso sangathe kuona? |
Yehova ali mu Kachisi wake woyera, Yehova, mpando wachifumu wake uli mu Mwamba; apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.
Mwayesera mtima wanga; mwandizonda usiku; mwandisuntha, simupeza kanthu; mwatsimikiza mtima kuti m'kamwa mwanga simudzalakwa.
Nkhope ya Yehova itsutsana nao akuchita zoipa, kudula chikumbukiro chao padziko lapansi.
Koma Yehova ananena naye, Anampangira munthu m'kamwa ndani? Kapena analenga munthu wosalankhula ndani, kapena wogontha, kapena wamaso, kapena wakhungu? Si ndine Yehova kodi?
Taonani, mkono wa Yehova sufupika, kuti sungathe kupulumutsa; khutu lake silili logontha, kuti silingamve;