Pakuti aona anzeru amafa, monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo, nasiyira ena chuma chao.
Masalimo 94:8 - Buku Lopatulika Zindikirani, opulukira inu mwa anthu; ndipo opusa inu, mudzachita mwanzeru liti? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zindikirani, opulukira inu mwa anthu; ndipo opusa inu, mudzachita mwanzeru liti? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mvetsani anthu opusa kwambirinu. Zitsiru inu, mudzakhala ndi nzeru liti? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Samalani, inu anthu opanda nzeru pakati pa anthu; zitsiru inu, kodi mudzakhala liti anzeru? |
Pakuti aona anzeru amafa, monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo, nasiyira ena chuma chao.
Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, opusa ndi kuda nzeru?
Ponyala nthambi zake zidzathyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; chifukwa chake Iye amene anawalenga sadzawachitira chisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima.
Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.