Kodi onse ochita zopanda pake sadziwa kanthu? Pakudya anthu anga monga akudya mkate, ndipo saitana pa Yehova.
Masalimo 94:5 - Buku Lopatulika Aphwanya anthu anu, Yehova, nazunza cholowa chanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Aphwanya anthu anu, Yehova, nazunza cholandira chanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amatswanya anthu anu, Inu Chauta, amazunza anthu anu osankhidwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amaphwanya anthu anu, Inu Yehova; amapondereza cholowa chanu. |
Kodi onse ochita zopanda pake sadziwa kanthu? Pakudya anthu anga monga akudya mkate, ndipo saitana pa Yehova.
Ananena mumtima mwao, Tiwapasule pamodzi; anatentha zosonkhaniramo za Mulungu zonse, m'dzikomo.
muti bwanji inu, amene mupsinja anthu anga, ndi kupera nkhope ya wosauka? Ati Ambuye, Yehova wa makamu.
Chifukwa chake kodi ndichitenji pano? Ati Yehova; popeza anthu anga achotsedwa popanda kanthu? Akuwalamulira awaliritsa, ati Yehova; ndipo dzina langa lichitidwa mwano tsiku lonse kosalekeza.
Koma maso ako ndi mtima wako sizisamalira kanthu koma kusirira, ndi kukhetsa mwazi wosachimwa, ndi kusautsa, ndi zachiwawa, kuti uzichite.
Chifukwa mukondwa, chifukwa musekerera, inu amene mulanda cholowa changa, chifukwa muli onenepa monga ng'ombe yaikazi yoponda tirigu, ndi kulira ngati akavalo olimba;
Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wandidya ine, wandiphwanya ine, wandiyesa ine ngati mbiya yopanda kanthu, wandimeza ngati ng'ona, wadzaza m'kamwa mwake ndi zotsekemera zanga, wanditaya ine.
Mwa iwe anapepula atate ndi mai, pakati pa iwe anamchitira mlendo momzunza, mwa iwe anazunza ana amasiye, ndi mkazi wamasiye.
Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri amphambu makumi asanu ndi limodzi, zovala chiguduli.
Ndipo ndinaona mkazi woledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu; ndipo ndinazizwa pakumuona iye ndi kuzizwa kwakukulu.