Taona, wodala munthu amene Mulungu amdzudzula; chifukwa chake usapeputsa kulanga kwa Wamphamvuyonse.
Masalimo 94:12 - Buku Lopatulika Wodala munthu amene mumlanga, Yehova; ndi kumphunzitsa m'chilamulo chanu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Wodala munthu amene mumlanga, Yehova; ndi kumphunzitsa m'chilamulo chanu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Chauta, ngwodala munthu amene mumamlangiza, amene mumamphunzitsa ndi malamulo anu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wodala munthu amene Inu Yehova mumamulangiza, munthu amene mumamuphunzitsa kuchokera mulamulo lanu; |
Taona, wodala munthu amene Mulungu amdzudzula; chifukwa chake usapeputsa kulanga kwa Wamphamvuyonse.
Mau a Yehova aitana mzinda, ndi wanzeru aopa dzina lanu; tamverani ndodo, ndi Iye amene anaiika.
Koma poweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi dziko lapansi.
Ndipo muzindikire m'mtima mwanu, kuti monga munthu alanga mwana wake, momwemo Yehova Mulungu wanu akulangani inu.
Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.