Masalimo 93:3 - Buku Lopatulika Mitsinje ikweza, Yehova, mitsinje ikweza mkokomo wao; mitsinje ikweza mafunde ao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mitsinje ikweza, Yehova, mitsinje ikweza mkokomo wao; mitsinje ikweza mafunde ao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Chauta, nyanja zazikulu zakwera, zikukokoma koopsa. Mafunde ake akuchita mkokomo waukulu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nyanja zakweza Inu Yehova, nyanja zakweza mawu ake; nyanja zakweza mafunde ake ochita mkokomo. |
Pali mtsinje, ngalande zake zidzakondweretsa mzinda wa Mulungu. Malo oyera okhalamo Wam'mwambamwamba.
Pakuti inu mudzatuluka ndi kukondwa, ndi kutsogozedwa ndi mtendere; mapiri ndi zitunda, zidzaimba zolimba pamaso panu, ndi mitengo yonse ya m'thengo idzaomba m'manja mwao.
Pakuti munandiponya mwakuya m'kati mwa nyanja, ndipo madzi anandizinga; mafunde anu onse a nyondonyondo anandimiza.
Ndipo njokayo inalavula m'kamwa mwake, madzi ngati mtsinje, potsata mkazi, kuti mkaziyo akakokoleredwe nao.
Ndipo anena ndi ine, Madziwo udawaona uko akhalako mkazi wachigololoyo ndiwo anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe.