Koma iwo akupatula kutsata njira zao zokhotakhota, Yehova adzawachotsa pamodzi ndi ochita zopanda pake. Mtendere ukhale pa Israele.
Masalimo 92:8 - Buku Lopatulika Koma Inu, Yehova, muli m'mwamba kunthawi yonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Inu, Yehova, muli m'mwamba kunthawi yonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu nokha Chauta, ndinu Wopambanazonse mpaka muyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Inu Yehova, ndinu wokwezedwa kwamuyaya. |
Koma iwo akupatula kutsata njira zao zokhotakhota, Yehova adzawachotsa pamodzi ndi ochita zopanda pake. Mtendere ukhale pa Israele.
Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi.
Yehova Wam'mwamba ndiye wamphamvu, wakuposa mkokomo wa madzi ambiri, ndi mafunde olimba a nyanja.
Tsopano ndidziwa kuti Yehova ali wamkulu ndi milungu yonse, pakuti momwe anadzikuza okha momwemo anawaposa.
Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkulu wopambana asamalira; ndipo alipo akulu ena oposa amenewo.