Mtima wake ngwochirikizika, sadzachita mantha, kufikira ataona chofuna iye pa iwo omsautsa.
Masalimo 92:11 - Buku Lopatulika Diso langa lapenya chokhumba ine pa iwo ondilalira, m'makutu mwanga ndamva chokhumba ine pa iwo akuchita zoipa akundiukira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Diso langa lapenya chokhumba ine pa iwo ondilalira, m'makutu mwanga ndamva chokhumba ine pa iwo akuchita zoipa akundiukira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Maso anga aona kuwonongeka kwa adani anga, makutu anga amva za kugwa kwa adani ondiwukira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Maso anga aona kugonjetsedwa kwa olimbana nane, makutu anga amva za kugwa kwa amaliwongo anga oyipa. |
Mtima wake ngwochirikizika, sadzachita mantha, kufikira ataona chofuna iye pa iwo omsautsa.
Anagawagawa, anapatsa aumphawi; chilungamo chake chikhalitsa kosatha; nyanga yake idzakwezeka ndi ulemu.
Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga; mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka.
Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko. Pakudulidwa oipa udzapenya.
Pakuti anandilanditsa m'nsautso yonse; ndipo ndapenya ndi diso langa icho ndakhumbira pa adani anga.