Mamawa onse ndidzadula oipa onse a m'dziko; kuduliratu onse akuchita zopanda pake kumzinda wa Yehova.
Masalimo 92:10 - Buku Lopatulika Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati; anandidzoza mafuta atsopano. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati; anandidzoza mafuta atsopano. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ine mwandilimbitsa ngati njati. Mwandidzoza ndi mafuta atsopano. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mwakweza nyanga yanga ngati nyanga ya njati; mafuta abwino akhuthulidwa pamutu wanga. |
Mamawa onse ndidzadula oipa onse a m'dziko; kuduliratu onse akuchita zopanda pake kumzinda wa Yehova.
Anagawagawa, anapatsa aumphawi; chilungamo chake chikhalitsa kosatha; nyanga yake idzakwezeka ndi ulemu.
Koma iwo akupatula kutsata njira zao zokhotakhota, Yehova adzawachotsa pamodzi ndi ochita zopanda pake. Mtendere ukhale pa Israele.
Ndipo anakweza nyanga ya anthu ake, chilemekezo cha okondedwa ake onse; ndiwo ana a Israele, anthu a pafupi pa Iye. Aleluya.
Ndipo zidaoneka zoyendamo madzi, nafukuka maziko a dziko lapansi, mwa kudzudzula kwanu, Yehova, mwa mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwanu.
Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga; mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka.
Mukonda chilungamo, ndipo mudana nacho choipa, chifukwa chake Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wadzoza inu ndi mafuta a chikondwerero koposa anzanu.
Popeza Inu ndinu ulemerero wa mphamvu yao; ndipo potivomereza Inu nyanga yathu idzakwezeka.
Koma chikhulupiriko changa ndi chifundo changa zidzakhala naye; ndipo nyanga yake idzakwezeka m'dzina langa.
Mulungu amtulutsa mu Ejipito; ali nayo mphamvu yonga ya njati; adzawadya amitundu, ndiwo adani ake. Nadzamphwanya mafupa ao, ndi kuwapyoza ndi mivi yake.
Adani anu onse, Yehova, atayike momwemo. Koma iwo akukonda Inu akhale ngati dzuwa lotuluka mu mphamvu yake. Ndipo dziko linapumula zaka makumi anai.
Ndipo Hana anapemphera, nati, Mtima wanga umyuka mokondwera kwa Yehova, nyanga yanga yakwezeka mwa Yehova; pakamwa panga pakula kwa adani anga; popeza ndikondwera m'chipulumutso chanu.
Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika; kumwamba Iye adzagunda pa iwo; Yehova adzaweruza malekezero a dziko. Ndipo adzapatsa mphamvu mfumu yake, nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wake.