Chomwecho Yehova anatumiza mliri pa Israele kuyambira m'mawa kufikira nthawi yoikika; ndipo anafapo anthu zikwi makumi asanu ndi awiri kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.
Masalimo 91:3 - Buku Lopatulika Pakuti adzakuonjola kumsampha wa msodzi, kumliri wosakaza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti adzakuonjola kumsampha wa msodzi, kumliri wosakaza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa wosaka, ndiponso ku mliri woopsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa mlenje ndi ku mliri woopsa; |
Chomwecho Yehova anatumiza mliri pa Israele kuyambira m'mawa kufikira nthawi yoikika; ndipo anafapo anthu zikwi makumi asanu ndi awiri kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.
M'dziko mukakhala njala, mukakhala mliri, mlaza, chinoni, dzombe, kapena kapuchi, adani ao akawamangira misasa m'dziko la mizinda yao, mukakhala mliri uliwonse, kapena nthenda;
Moyo wathu unaonjoka ngati mbalame mu msampha wa msodzi; msampha unathyoka ndi ife tinaonjoka.
Mundisunge ndisagwe mumsampha ananditcherawo, ndisakodwe m'makwekwe a iwo ochita zopanda pake.
Indedi Mulungu adzaphwanya mutu wa adani ake, pakati pamutu pa iye woyendabe m'kutsutsika kwake.
mpaka muvi ukapyoza mphafa yake; amtsata monga mbalame yothamangira msampha; osadziwa kuti adzaononga moyo wake.
Pakuti munthu sadziwatu mphindi yake; monga nsomba zigwidwa mu ukonde woipa, ndi mbalame zikodwa mumsampha, momwemo ana a anthu amagwidwa ndi nthawi ya tsoka, ngati msampha umene uwagwera modzidzimuka.
Efuremu ndiye wozonda kwa Mulungu wanga; kunena za mneneri, msampha wa msodzi uli m'njira zake zonse, ndi udani m'nyumba ya Mulungu wake.
Kodi mbalame idzakodwa mumsampha pansi popanda msampha woitchera? Kodi msampha ufwamphuka pansi wosakola kanthu?
Koma iwo akufuna kukhala achuma amagwa m'chiyesero ndi m'msampha, ndi m'zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m'chionongeko ndi chitayiko.
ndipo akadzipulumutse kumsampha wa mdierekezi, m'mene anagwidwa naye, kuchifuniro chake.