Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja; ndipo zaka zanga zili ngati chabe pamaso panu, Indedi munthu aliyense angakhale wokhazikika, ali chabe konse.
Masalimo 90:4 - Buku Lopatulika Pakuti pamaso panu zaka zikwi zikhala ngati dzulo, litapita, ndi monga ulonda wa usiku. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti pamaso panu zaka zikwi zikhala ngati dzulo, litapita, ndi monga ulonda wa usiku. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti zaka chikwi chimodzi pamaso panu zili ngati dzulo chabe, kapena ngati kamphindi chabe kausiku. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti zaka 1,000 pamaso panu zili ngati tsiku limene lapita kapena ngati kamphindi ka usiku. |
Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja; ndipo zaka zanga zili ngati chabe pamaso panu, Indedi munthu aliyense angakhale wokhazikika, ali chabe konse.
Ndipo kunali, ulonda wa mamawa, Yehova ali m'moto ndi m'mtambo njo anapenyera pa ulendo wa Aejipito, nauvuta ulendo wa Aejipito.
Koma dziwani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yiti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibooledwe.
Koma ichi chimodzi musaiwale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka chikwi, ndi zaka chikwi ngati tsiku limodzi.
Motero Gideoni ndi amuna zana anali naye anafikira ku chilekezero cha misasa poyambira ulonda wa pakati, atasintha alonda tsopano apa; ndipo anaomba malipenga, naphwanya mbiya zokhala m'manja mwao.