Koma kwa munthu anati, Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.
Masalimo 90:12 - Buku Lopatulika Mutidziwitse kuwerenga masiku athu motero, kuti tikhale nao mtima wanzeru. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mutidziwitse kuwerenga masiku athu motero, kuti tikhale nao mtima wanzeru. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono tiphunzitseni kuŵerenga masiku athu, kuti tikhale ndi mtima wanzeru. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tiphunzitseni kuwerenga masiku athu molondola, kuti tikhale ndi mtima wanzeru. |
Koma kwa munthu anati, Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.
Yehova, mundidziwitse chimaliziro changa, ndi mawerengedwe a masiku anga ndi angati; ndidziwe malekezero anga.
Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja; ndipo zaka zanga zili ngati chabe pamaso panu, Indedi munthu aliyense angakhale wokhazikika, ali chabe konse.
Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golide, kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?
Kunka kunyumba ya maliro kupambana kunka kunyumba ya madyerero; pakuti kujako ndi matsiriziro a anthu onse; ndipo omwe ali ndi moyo adzakumbukirapo.
Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.
Tiyenera kugwira ntchito za Iye wondituma Ine, pokhala pali msana; ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira ntchito.