Masalimo 9:17 - Buku Lopatulika Oipawo adzabwerera kumanda, inde amitundu onse akuiwala Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Oipawo adzabwerera kumanda, inde amitundu onse akuiwala Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono anthu oipa adzapita ku dziko la anthu akufa, ndiye kuti anthu onse amene amakana Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Oyipa amabwerera ku manda, mitundu yonse imene imayiwala Mulungu. |
Momwemo mayendedwe a onse oiwala Mulungu; ndi chiyembekezo cha onyoza Mulungu; chidzatayika.
Tikadaiwala dzina la Mulungu wathu, ndi kutambasulira manja athu kwa mulungu wachilendo;
Aikidwa m'manda ngati nkhosa; mbusa wao ndi imfa. Ndipo m'mawa mwake oongoka mtima adzakhala mafumu ao; ndipo maonekedwe ao adzanyekera kumanda, kuti pokhala pake padzasowa.
Dziwitsani ichi inu oiwala Mulungu, kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi.
Tsoka kwa woipa! Kudzamuipira; chifukwa kuti mphotho ya manja ake idzapatsidwa kwa iye.
Ndipo manda akuza chilakolako chake, natsegula kukamwa kwake kosayeseka; ndi ulemerero wao, ndi unyinji wao, ndi phokoso lao, ndi iye amene akondwerera mwa iwo atsikira mommo.
Ichi ndi chogwera chako, gawo la muyeso wako wa kwa Ine, ati Yehova; chifukwa wandiiwala Ine, ndi kukhulupirira zonama.
Pakuti anthu anga andiiwala Ine, afukizira zopanda pake; aphunthwitsa iwo m'njira zao, m'njira zakale, kuti ayende m'njira za m'mbali, m'njira yosatundumuka;
Kodi angathe namwali kuiwala zokometsera zake, kapena mkwatibwi zovala zake? Koma anthu anga andiiwala Ine masiku osawerengeka.
Mau amveka pa mapiri oti see, kulira ndi kupempha kwa ana a Israele; pakuti anaipitsa njira yao, naiwala Yehova Mulungu wao.
Ndipo udzaipsidwa mwa iwe wekha pamaso pa amitundu; motero udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Ndipo ndidzamlanga chifukwa cha masiku a Abaala amene anawafukizira, navala mphete za m'mphuno, ndi zokometsera zake, natsata omkonda, nandiiwala Ine, ati Yehova.
Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.