Ndipo tsono, Yehova Mulungu wathu, mutipulumutse m'dzanja lake, kuti adziwe maufumu onse a dziko lapansi kuti Inu ndinu Yehova Mulungu, Inu nokhanokha.
Masalimo 9:16 - Buku Lopatulika Anadziwika Yehova, anachita kuweruza, woipayo anakodwa ndi ntchito ya manja ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anadziwika Yehova, anachita kuweruza, woipayo anakodwa ndi ntchito ya manja ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta wadziwulula yekha, pakuweruza molungama, koma anthu oipa akodwa mu msampha wotcha iwo omwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova amadziwika ndi chilungamo chake; oyipa akodwa ndi ntchito za manja awo. Higayoni. Sela |
Ndipo tsono, Yehova Mulungu wathu, mutipulumutse m'dzanja lake, kuti adziwe maufumu onse a dziko lapansi kuti Inu ndinu Yehova Mulungu, Inu nokhanokha.
Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa; moto ndi miyala ya sulufure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'chikho chao.
Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.
Ndipo pamene Farao anayandikira ana a Israele anatukula maso ao, taonani, Aejipito alinkutsata pambuyo pao; ndipo anaopa kwambiri; ndi ana a Israele anafuulira kwa Yehova.
Ndipo Israele anaiona ntchito yaikulu imene Yehova anachitira Aejipito, ndipo anthuwo anaopa Yehova; nakhulupirira Yehova ndi mtumiki wake Mose.
Ndipo ndidzalimbitsa mtima wake wa Farao kuti awalondole; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao ndi pa nkhondo yake yonse; pamenepo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndipo anachita chomwecho.
Ndipo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakutambasula Ine dzanja langa pa Aejipito, ndikutulutsa ana a Israele pakati pao.
Chifukwa chake mau a Yehova adzakhala kwa iwo langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono; kuti ayende ndi kugwa chambuyo, ndi kuthyoka, ndi kukodwa mumsampha, ndi kugwidwa.
Pamenepo mfumu Dariusi analembera kwa anthu, mitundu ya anthu, ndi a manenedwe onse okhala padziko lonse lapansi, Mtendere uchulukire inu.
Pamenepo anati Adoni-Bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikulu za m'manja ndi m'mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinachita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye ku Yerusalemu, nafa iye komweko.
Lero lino Yehova adzakupereka iwe m'dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukuchotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israele kuli Mulungu.