Masalimo 9:15 - Buku Lopatulika Amitundu anagwa m'mbuna imene anaikumba, lakodwa phazi lao muukonde anautchera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Amitundu anagwa m'mbuna imene anaikumba, lakodwa phazi lao muukonde anautcha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akunja agwera m'mbuna yokumba iwo omwe. Phazi lao lakodwa mu ukonde wobisika wotcha iwo omwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mitundu ya anthu yagwa mʼdzenje limene yakumba; mapazi awo akodwa mu ukonde umene anawubisa. |
Tsopano ndidziwa kuti Yehova apulumutsa wodzozedwa wake; adzamvomereza mu Mwamba mwake moyera ndi mphamvu ya chipulumutso cha dzanja lake lamanja.
Chimgwere modzidzimutsa chionongeko; ndipo ukonde wake umene anautcha umkole yekha mwini, agwemo, naonongeke m'mwemo.
Ananditchera ukonde apo ndiyenda; moyo wanga wawerama. Anandikumbira mbuna patsogolo panga; anagwa m'kati mwake iwo okha.
Ndipo anawabwezera zopanda pake zao, nadzawaononga m'choipa chao; Yehova Mulungu wathu adzawaononga.