Adzafotokoza ndani ntchito zamphamvu za Yehova, adzamveketsa ndani chilemekezo chake chonse?
Masalimo 9:14 - Buku Lopatulika Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse; pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni, ndidzakondwera nacho chipulumutso chanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse; pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni, ndidzakondwera nacho chipulumutso chanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa kuti ndithe kuyamika ntchito zanu zonse, pakati pa anthu anu a mu Ziyoni. Zoonadi ndidzakondwa chifukwa mwandipulumutsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kuti ndilengeze za matamando anu pa zipata za ana aakazi a Ziyoni, kuti pamenepo ndikondwere ndi chipulumutso chanu. |
Adzafotokoza ndani ntchito zamphamvu za Yehova, adzamveketsa ndani chilemekezo chake chonse?
Koma ine ndakhulupirira pa chifundo chanu; mtima wanga udzakondwera nacho chipulumutso chanu.
Tidzafuula mokondwera mwa chipulumutso chanu, ndipo m'dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera; Yehova akwaniritse mapempho ako onse.
Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukulu, zowinda zanga ndidzazichita pamaso pa iwo akumuopa Iye.
Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine, pakuti ndinkapita ndi unyinji wa anthu, ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu, ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika, ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.
Potero ife anthu anu ndi nkhosa zapabusa panu tidzakuyamikani kosatha; tidzafotokozera chilemekezo chanu ku mibadwomibadwo.
Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali mu Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;
Ndipo tsopano, taona kulira kwa ana a Israele kwandifikira; ndapenyanso kupsinjika kumene Aejipito awapsinja nako.
awa ndiwo mau amene Yehova wanena za iye, Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza iwe ndi kuseka iwe ndi chiphwete; mwana wamkazi wa Yerusalemu wapukusa mutu wake pambuyo pako.
Taonani, Yehova walalikira kufikira malekezero a dziko lapansi. Nenani kwa mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona chipulumutso chako chifika; taona mphotho yake ali nayo, ndi ntchito yake ili pamaso pake.
Nyamuka nupunthe, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti ndidzasanduliza nyanga yako ikhale yachitsulo, ndi ziboda zako zikhale zamkuwa; ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu; ndipo uzipereka chiperekere phindu lao kwa Yehova, ndi chuma chao kwa Ambuye wa dziko lonse lapansi.
Ndipo Hana anapemphera, nati, Mtima wanga umyuka mokondwera kwa Yehova, nyanga yanga yakwezeka mwa Yehova; pakamwa panga pakula kwa adani anga; popeza ndikondwera m'chipulumutso chanu.