Masalimo 9:11 - Buku Lopatulika Imbirani zoyamika Yehova, wokhala ku Ziyoni; lalikirani mwa anthu ntchito zake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Imbirani zoyamika Yehova, wokhala ku Ziyoni; lalikirani mwa anthu ntchito zake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Imbani nyimbo zotamanda Chauta amene amakhala ku Ziyoni. Lalikani za ntchito zake kwa anthu a mitundu yonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Imbani nyimbo zamatamando kwa Yehova, ali pa mpando waufumu mu Ziyoni; lengezani pakati pa mitundu ya anthu zimene wachita. |
Nenani mwa amitundu, Yehova achita ufumu; dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke; adzaweruza mitundu ya anthu molunjika.
Ndipo adzayankhanji amithenga a amitundu? Kuti Yehova wakhazikitsa Ziyoni, ndipo m'menemo anthu ake ovutidwa adzaona pobisalira.
ndipo ndinazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa; kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndi Ine mwa iwo.
Komatu mwayandikira kuphiri la Ziyoni, ndi mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wochuluka wa angelo,
Ndipo ndinapenya, taonani, Mwanawankhosayo alikuimirira paphiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, akukhala nalo dzina lake ndi dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pao.