Masalimo 88:3 - Buku Lopatulika Pakuti mzimu wanga wadzala nao mavuto, ndi moyo wanga wayandikira kumanda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti mzimu wanga wadzala nao mavuto, ndi moyo wanga wayandikira kumanda. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti mtima wanga ndi wodzaza ndi mavuto, moyo wanga ukuyandikira ku malo a anthu akufa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti ndili ndi mavuto ambiri ndipo moyo wanga ukuyandikira ku manda. |
Yehova, imvani chilungamo, mverani mfuu wanga; tcherani khutu ku pemphero langa losatuluka m'milomo ya chinyengo.
Tsiku la nsautso yanga ndinafuna Ambuye. Dzanja langa linatambalika usiku, losaleka; mtima wanga unakana kutonthozedwa.
Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeze.