Masalimo 86:7 - Buku Lopatulika Tsiku la msauko wanga ndidzaitana Inu; popeza mudzandivomereza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsiku la msauko wanga ndidzaitana Inu; popeza mudzandivomereza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa tsiku lamavuto ndimakuitanani, pakuti mumayankha mapemphero anga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa tsiku la mavuto anga ndidzayitana Inu, pakuti Inu mudzandiyankha. |
Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga. M'njira ndiyendamo ananditchera msampha.
Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu; tcherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga.
M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova, ndipo ndinakuwira Mulungu wanga; mau anga anawamva mu Kachisi mwake, ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m'makutu mwake.
Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.
Ndipo anati, Ndinaitana Yehova m'nsautso wanga, ndipo anandiyankha ine; ndinafuula ndili m'mimba ya manda, ndipo munamva mau anga.
Ndipo pokhala Iye m'chipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lake linakhala ngati madontho aakulu a mwazi alinkugwa pansi.
Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,