Mundimvetse chifundo chanu mamawa; popeza ndikhulupirira Inu: Mundidziwitse njira ndiyendemo; popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.
Masalimo 86:4 - Buku Lopatulika Kondwetsani moyo wa mtumiki wanu; pakuti ndikwezera moyo wanga kwa Inu, Ambuye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kondwetsani moyo wa mtumiki wanu; pakuti ndikwezera moyo wanga kwa Inu, Ambuye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sangalatsani mtima wa ine mtumiki wanu, pakuti ndikupereka mtima wanga kwa Inu Ambuye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Bweretsani chimwemwe kwa mtumiki wanu, Ambuye, pakuti ndimadalira Inu. |
Mundimvetse chifundo chanu mamawa; popeza ndikhulupirira Inu: Mundidziwitse njira ndiyendemo; popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.
Khulupirirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu, tsanulirani mitima yanu pamaso pake. Mulungu ndiye pothawirapo ife.
ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.
Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala kunthawi zonse ndi ichi ndichilenga; pakuti taonani, ndilenga Yerusalemu wosangalala, ndi anthu ake okondwa.