Masalimo 86:2 - Buku Lopatulika Sungani moyo wanga pakuti ine ndine wokondedwa wanu; Inu Mulungu wanga, pulumutsani mtumiki wanu wokhulupirira Inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Sungani moyo wanga pakuti ine ndine wokondedwa wanu; Inu Mulungu wanga, pulumutsani mtumiki wanu wokhulupirira Inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sungani moyo wanga, pakuti ndine womvera Inu. Pulumutseni ine mtumiki wanu amene ndimadalira Inu. Inu ndinu Mulungu wanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yangʼanirani moyo wanga, pakuti ndine wodzipereka kwa Inu. Inu ndinu Mulungu wanga; pulumutsani mtumiki wanu amene amadalira Inu. Inu ndinu Mulungu wanga. |
Koma ine ndakhulupirira pa chifundo chanu; mtima wanga udzakondwera nacho chipulumutso chanu.
Ndipo mwa chifundo chanu mundidulire adani anga, ndipo muononge onse akusautsa moyo wanga; pakuti ine ndine mtumiki wanu.
Ndakhulupirira Inu, Yehova, ndikhale wopanda manyazi nthawi zonse, mwa chilungamo chanu ndipulumutseni ine.
Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.
Koma dziwani kuti Yehova anadzipatulira yekha womkondayo, adzamva Yehova m'mene ndimfuulira Iye.
Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamchitira ulemu iyeyu.
Sindikhalanso m'dziko lapansi, koma iwo ali m'dziko lapansi, ndipo Ine ndidza kwa Inu. Atate Woyera, sungani awa m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine, kuti akhale mmodzi, monga Ife.
Adzasunga mapazi a okondedwa ake, koma oipawo adzawakhalitsa chete mumdima; pakuti palibe munthu adzapambana ndi mphamvu.