Mwapenya; pakuti mumayang'anira chivutitso ndi chisoni kuti achipereke m'manja mwanu; waumphawi adzipereka kwa Inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake.
Masalimo 86:1 - Buku Lopatulika Tcherani khutu lanu Yehova, mundiyankhe; pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tcherani khutu lanu Yehova, mundiyankhe; pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tcherani khutu, Inu Chauta, ndipo mundiyankhe, pakuti ndine wosauka ndi wosoŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndimvereni Yehova ndipo mundiyankhe, pakuti ndine wosauka ndi wosowa. |
Mwapenya; pakuti mumayang'anira chivutitso ndi chisoni kuti achipereke m'manja mwanu; waumphawi adzipereka kwa Inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake.
Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu; tcherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga.
Munditcherere khutu lanu; ndipulumutseni msanga. Mundikhalire ine thanthwe lolimba, nyumba yamalinga yakundisunga.
Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nampulumutsa m'masautso ake onse.
Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi; koma Ambuye andikumbukira ine. Inu ndinu mthandizi wanga, ndi Mpulumutsi wanga, musamachedwa, Mulungu wanga.
Tcherani makutu anu, Yehova, nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimuone; ndi kumva mau onse a Senakeribu, amene watumiza kumtonza Mulungu wamoyo.
Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.
Mulungu wanga, tcherani khutu, nimumvere, tsegulani maso anu, nimupenye zopasuka zathu, ndi mzinda udatchedwawo dzina lanu; pakuti dzina lanu; pakuti sititula mapembedzero athu pamaso panu, chifukwa cha ntchito zathu zolungama, koma chifukwa cha zifundo zanu zochuluka.
Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,
Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankhe osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?