Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine; ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.
Masalimo 85:7 - Buku Lopatulika Tionetseni chifundo chanu, Yehova, tipatseni chipulumutso chanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tionetseni chifundo chanu, Yehova, tipatseni chipulumutso chanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tiwonetseni chikondi chanu chosasinthika, Inu Chauta, ndipo mutipulumutse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tionetseni chikondi chanu chosatha, Inu Yehova, ndipo tipatseni chipulumutso chanu. |
Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine; ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.
Atero Yehova: M'malo muno, m'mene muti, Ndi bwinja, mopanda munthu, mopanda nyama, m'mizinda ya Yuda, m'makwalala a Yerusalemu, amene ali bwinja, opanda munthu, opanda wokhalamo, opanda nyama,
mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.
Ndipo ndidzakuchitirani inu chifundo, kuti iye akuchitireni inu chifundo, nakubwezereni inu kudziko lanu.