Masalimo 85:4 - Buku Lopatulika Mutibweze, Mulungu wa chipulumutso chathu, nimuletse udani wanu wa pa ife. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mutibweze, Mulungu wa chipulumutso chathu, nimuletse udani wanu wa pa ife. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mutibwezerenso mwakale, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, ndipo mutichotsere mkwiyo wanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tibwezeretseninso mwakale Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, ndipo mutichotsere mkwiyo wanu. |
Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?
Koma Iye pokhala ngwa chifundo, anakhululukira choipa, osawaononga; nabweza mkwiyo wake kawirikawiri, sanautse ukali wake wonse.
Tsiku lomwelo udzati, Ndikuyamikani inu Yehova; pakuti ngakhale munandikwiyira, mkwiyo wanu wachoka, ndipo mutonthoza mtima wanga.
Kumva ndamva Efuremu alinkulirira kotero, Mwandilanga ine, ndipo ndalangidwa, monga mwanawang'ombe wosazolowera goli; munditembenuze ine, ndipo ine ndidzatembenuka; pakuti inu ndinu Yehova Mulungu wanga.
Mutitembenuzire kwa Inu, Yehova, ndipo tidzatembenuzidwadi, mukonzenso masiku athu ngati kale lija.
Ambuye, monga mwa chilungamo chanu chonse, mkwiyo wanu ndi ukali wanu zitembenuketu, zichoke kumzinda wanu Yerusalemu, phiri lanu lopatulika; pakuti mwa zochimwa zathu, ndi mphulupulu za makolo athu, Yerusalemu ndi anthu anu asanduka chotonza cha onse otizungulira.
Sindidzachita mkwiyo wanga waukali, sindidzabwerera kuononga Efuremu; pakuti Ine ndine Mulungu, si munthu ai; Woyera wa pakati pako; ndipo sindidzalowa m'mzinda.
Koma ine, ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa chipulumutso changa; Mulungu wanga adzandimvera.
Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse.
Inu mulambira chimene simuchidziwa; ife tilambira chimene tichidziwa; pakuti chipulumutso chichokera kwa Ayuda.
Ndipo anamuunjikira mulu waukulu wamiyala, wokhalako kufikira lero lino; ndipo Yehova anatembenuka kusiya mkwiyo wake waukulu. Chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo, Chigwa cha Akori, mpaka lero lino.