Ndipo anati, Chifukwa chake tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lili chilili m'mbali mwake, ku dzanja lamanja ndi lamanzere.
Masalimo 84:1 - Buku Lopatulika Pokhala Inu mpotikonda ndithu, Yehova wa makamu! Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pokhala Inu mpotikonda ndithu, Yehova wa makamu! Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Malo amene mumakhalamo, Inu Chauta Wamphamvuzonse, ndi okoma kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Malo anu okhalamo ndi okomadi, Inu Yehova Wamphamvuzonse! |
Ndipo anati, Chifukwa chake tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lili chilili m'mbali mwake, ku dzanja lamanja ndi lamanzere.
Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse zili pomwepo, nyanja ndi zonse zili m'mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu lakumwamba lilambira Inu.
Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.
Adzakhuta kwambiri ndi zonona za m'nyumba mwanu, ndipo mudzawamwetsa mu mtsinje wa zokondweretsa zanu.
Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.
Tumizirani kuunika kwanu ndi choonadi chanu zinditsogolere; zindifikitse kuphiri lanu loyera, kumene mukhala Inuko.
Yehova, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga padziko lonse lapansi! Inu amene munaika ulemerero wanu pa thambo la kumwamba.