Masalimo 83:15 - Buku Lopatulika Momwemo muwatsate ndi namondwe, nimuwaopse ndi kamvulumvulu wanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Momwemo muwatsate ndi namondwe, nimuwaopse ndi kamvulumvulu wanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa momwemonso Inu muŵapirikitse ndi mkuntho, ndipo muŵaopseze ndi kamvulumvulu wanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kotero muwathamangitse ndi mphepo yamkuntho, ndi kuwachititsa mantha ndi namondwe. |
Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa; moto ndi miyala ya sulufure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'chikho chao.
Adzafika Mulungu wathu, ndipo sadzakhala chete. Moto udzanyeka pankhope pake, ndipo pozungulira pake padzasokosera kwakukulu.
Ndipo ndidzayesa chiweruziro chingwe choongolera, ndi chilungamo chingwe cholungamitsira chilili; ndipo matalala adzachotsa pothawirapo mabodza, ndi madzi adzasefukira mobisalamo.
Ndipo Yehova adzamveketsa mau ake a ulemerero, ndipo adzaonetsa kumenya kwa dzanja lake, ndi mkwiyo wake waukali, ndi lawi la moto wonyambita, ndi kuomba kwa mphepo, ndi mkuntho ndi matalala.
nuziti kwa dziko la Israele, Atero Yehova, Taona Ine ndine wotsutsana nawe, ndidzasolola lupanga langa m'chimake, ndi kukulikhira olungama ndi oipa.
ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu.
Pakuti simunayandikire phiri lokhudzika, ndi lakupsa moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe,