Masalimo 83:13 - Buku Lopatulika Mulungu wanga, muwaike akhale ngati mungu; ngati ziputu zomka ndi mphepo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mulungu wanga, muwaike akhale ngati mungu; ngati ziputu zomka ndi mphepo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Mulungu wanga, muŵasandutse ngati fumbi louluka ndi kamvulumvulu, akhale ngati mankhusu ouluka ndi mphepo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Muwasandutse fumbi lowuluka, Inu Mulungu wanga, ngati mankhusu owuluka ndi mphepo. |
Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine? Mukhaliranji kutali kwa chipulumutso changa, ndi kwa mau a kubuula kwanga?
Ndipo ndi ukulu wanu waukulu mwapasula akuukira Inu; mwatumiza mkwiyo wanu, unawanyeketsa ngati chiputu.
Inde sanaokedwe, inde sanafesedwe; inde, muzu wao sunazike pansi; koma Iye anawaombetsera mphepo, ndipo afota, ndipo kamvulumvulu awachotsa monga chiputu.
Ndani anautsa wina wochokera kum'mawa, amene amuitana m'chilungamo, afike pa phazi lake? Iye apereka amitundu patsogolo pake, namlamuliritsa mafumu; nawapereka monga fumbi kulupanga lake, monga chiputu chouluzidwa ku uta wake.
Popeza wanena, Mitundu iwiri iyi ya anthu ndi maiko awiri awa adzakhala anga, tidzakhala nao ngati cholowa chathu, angakhale Yehova anali komweko;
Atero Ambuye Yehova, Popeza mdani ananena za inu, Ha! Ingakhale misanje yakale ili yathu, cholowa chathu;
chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.