ndi thupi la Yezebele lidzakhala ngati ndowe pamunda m'dera la Yezireele, kuti sadzati, Ndi Yezebele uyu.
Masalimo 83:10 - Buku Lopatulika amene anaonongeka ku Endori; anakhala ngati ndowe ya kumunda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 amene anaonongeka ku Endori; anakhala ngati ndowe ya kumunda. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa amene adaŵaononga ku Endori, ndi kuŵasandutsa ndoŵe m'nthaka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amene anawonongedwa ku Endori ndi kukhala ngati zinyalala. |
ndi thupi la Yezebele lidzakhala ngati ndowe pamunda m'dera la Yezireele, kuti sadzati, Ndi Yezebele uyu.
Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za kumlengalenga, ndi zilombo za dziko lapansi.
ndipo udzawayanika padzuwa, ndi pamwezi, ndi pa khamu lonse la kuthambo, limene analikonda, ndi kulitumikira, ndi kulitsata, ndi kulifuna, ndi kuligwadira; sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ndowe panthaka.
Ndipo ndidzatengera anthu zowapsinja, kuti adzayenda ngati anthu akhungu, popeza anachimwira Yehova; ndi mwazi wao udzatsanulidwa ngati fumbi, ndi nyama yao idzanga ndowe.
Ndipo mu Isakara ndi mu Asere Manase anali nao Beteseani ndi midzi yake, ndi Ibleamu ndi midzi yake, ndi nzika za Dori ndi midzi yake, ndi nzika za Endori ndi midzi yake, ndi nzika za Taanaki ndi midzi yake, ndi nzika za Megido ndi midzi yake; dziko la mapiri atatu.
Ndipo Yehova anaononga Sisera ndi magaleta onse ndi gulu lankhondo lonse, ndi lupanga lakuthwa pamaso pa Baraki; koma Sisera anatsika pagaleta nathawa choyenda pansi.
Koma Baraki anatsata magaleta ndi gululo mpaka Haroseti wa amitundu; ndi gulu lonse lankhondo la Sisera linagwa ndi lupanga lakuthwa, sanatsale munthu ndi mmodzi yense.
Mtsinje wa Kisoni unawakokolola, mtsinje uja wakale, mtsinje wa Kisoni. Yenda mwamphamvu, moyo wangawe.
Ndipo anagwira akalonga awiri a Midiyani, Orebu ndi Zeebu; namupha Orebu ku thanthwe la Orebu; ndi Zeebu anamupha ku choponderamo mphesa cha Zeebu, nalondola Amidiyani; ndipo anadza nayo mitu ya Orebu ndi Zeebu kwa Gideoni tsidya lija la Yordani.
Tsono Saulo anati kwa anyamata ake, Mundifunire mkazi wobwebweta, kuti ndimuke kwa iye ndi kumfunsira. Ndipo anyamata ake anati kwa iye, Onani ku Endori kuli mkazi wobwebweta.