Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 80:8 - Buku Lopatulika

Mudatenga mpesa kuchokera ku Ejipito, munapirikitsa amitundu ndi kuuoka uwu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Mudatenga mpesa kuchokera ku Ejipito, munapirikitsa amitundu ndi kuuoka uwu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mudatulutsa mpesa wanu Israele m'dziko la Ejipito. Mudapirikitsa mitundu ina ya anthu kuti muubzale mpesawo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Munatulutsa mpesa kuchoka ku Igupto; munathamangitsa anthu a mitundu ina ndi kuwudzala mpesawo.

Onani mutuwo



Masalimo 80:8
16 Mawu Ofanana  

Yehova, musandichititse manyazi; pakuti ndafuulira kwa Inu, oipa achite manyazi, atonthole m'manda.


Inu munapirikitsa amitundu ndi dzanja lanu, koma iwowa munawaoka; munasautsa mitundu ya anthu, ndipo munawaingitsa.


Mwaonetsa anthu anu zowawa, mwatimwetsa vinyo wotinjenjemeretsa.


Ndipo anapirikitsa amitundu pamaso pao, nawagawira cholowa chao, ndi muyeso, nakhalitsa mafuko a Israele m'mahema mwao.


Abusa ambiri aononga munda wanga wampesa, apondereza gawo langa, pondikondweretsa apayesa chipululu chopanda kanthu.


Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pake, ya mpesa wachilendo?


Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ngati mtengo wampesa pakati pa mitengo ya kunkhalango ndauponya kumoto ukhale nkhuni, momwemo ndidzapereka okhala mu Yerusalemu.


Ndipo inaphuka, nikhala mpesa wotambalala waufupi msinkhu, nthambi zake zinapindikira momwe, ndi mizu yake pansi pake, nikhala mpesa, nuonetsa nthambi ndi kuphuka mphukira.


Mai wako ananga mpesa wookedwa kumadzi; muja anakhala mumtendere unabala zipatso, wodzala ndi nthambi, chifukwa cha madzi ambiri.


Chimenenso makolo athu akudza m'mbuyo, analowa nacho ndi Yoswa polandira iwo zao za amitundu, amene Mulungu anawaingitsa pamaso pa makolo athu, kufikira masiku a Davide;


nzika zonse za kumapiri kuyambira Lebanoni, mpaka Misirefoti-Maimu, Asidoni onse; ndidzawainga pamaso pa ana a Israele, koma limeneli uwagawire Aisraele, likhale cholowa chao, monga ndinakulamulira.