Koma Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapolo Mwamoniyo, ndi Gesemu Mwarabu, anamva natiseka pwepwete, natipeputsa, nati, Chiyani ichi muchichita? Mulikupandukira mfumu kodi?
Masalimo 80:7 - Buku Lopatulika Mulungu wa makamu, mutibweze; nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mulungu wa makamu, mutibweze; nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Mulungu Wamphamvuzonse, tibwezereni mwakale, mutiwonetse nkhope yoŵala, kuti ife tipulumuke. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tibwezereni mwakale Inu Mulungu Wamphamvuzonse, nkhope yanu itiwalire kuti tipulumutsidwe. |
Koma Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapolo Mwamoniyo, ndi Gesemu Mwarabu, anamva natiseka pwepwete, natipeputsa, nati, Chiyani ichi muchichita? Mulikupandukira mfumu kodi?
Pakuti atero Ambuye, Yehova Woyera wa Israele, M'kubwera ndi m'kupuma inu mudzapulumutsidwa; m'kukhala chete ndi m'kukhulupirira mudzakhala mphamvu yanu; ndipo simunafune.
Inu mukomana ndi iye amene akondwerera, nachita chilungamo, iwo amene akumbukira Inu m'njira zanu; taonani Inu munakwiya, ndipo ife tinachimwa; takhala momwemo nthawi yambiri, kodi tidzapulumutsidwa?
Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati?
kuti kupenya apenye, koma asazindikire; ndipo kumva amve, koma asadziwitse; kuti pena angatembenuke, ndi kukhululukidwa.