Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine, pakuti ndinkapita ndi unyinji wa anthu, ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu, ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika, ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.
Masalimo 80:6 - Buku Lopatulika Mutiika kuti atilimbirane anzathu; ndipo adani athu atiseka mwa iwo okha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mutiika kuti atilimbirane anzathu; ndipo adani athu atiseka mwa iwo okha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwaŵasandutsa chinthu chonyozeka kwa anzathu a mitundu ina, ndipo adani athu akakhala pamodzi, amangotiseka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwachititsa kuti tikhale gwero la mikangano pakati pa anansi athu, ndipo adani athu akutinyoza. |
Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine, pakuti ndinkapita ndi unyinji wa anthu, ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu, ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika, ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.
Chifukwa chake upereketu zikole kwa mbuyanga, mfumu ya Asiriya, ndipo ine ndidzakupatsa iwe akavalo zikwi ziwiri, ngati iwe udzaona okwerapo.
Ndani amene, iwe wamtonza ndi kumlalatira? Ndani amene iwe wakwezera mau ako ndi kutukulira maso ako kumwamba? Ndiye Woyera wa Israele.
Kalanga ine, amai, pakuti mwandibala ine munthu wandeu, munthu wakutetana nalo dziko lonse lapansi! Sindinakongoletsa paphindu, anthu sanandikongoletse paphindu; koma iwo onse anditemberera.
Kodi sunaseke Israele? Kodi iye anapezedwa mwa mbala? Pakuti nthawi zonse unena za iye, upukusa mutu.
chifukwa chake, mapiri inu a Israele, imvani mau a Ambuye Yehova. Atero Ambuye Yehova kunena ndi mapiri, ndi zitunda, ndi mitsinje, ndi zigwa, ndi zipululu zopasuka, ndi mizinda yamabwinja, imene yakhala chakudya ndi choseketsa amitundu otsala akuzungulira;
Ndipo iwo akukhala padziko adzakondwerera, nasekerera, nadzatumizirana mitulo; popeza aneneri awa awiri anazunza iwo akukhala padziko.
Ndipo kunali, pakukondwera mitima yao, anati, Kaitaneni Samisoni, atisewerere. Naitana Samisoni m'kaidi; nasewera iye pamaso pao; ndipo anamuka iye pakati pa mizati.