Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 80:5 - Buku Lopatulika

Munawadyetsa mkate wa misozi, ndipo munawamwetsa misozi yambiri.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Munawadyetsa mkate wa misozi, ndipo munawamwetsa misozi yambiri.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mwaŵadyetsa chisoni ngati chakudya, mwaŵapatsa misozi ngati chakumwa.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mwawadyetsa buledi wa misozi; mwachitisa iwo kumwa misozi yodzaza mbale.

Onani mutuwo



Masalimo 80:5
9 Mawu Ofanana  

Zimene moyo wanga ukana kuzikhudza zikunga chakudya chosakolera kwa ine.


Pakuti ndadya mapulusa ngati mkate, ndi kusakaniza chomwera changa ndi misozi,


Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa, usana ndi usiku; pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?


Mulungu, munatitayiranji chitayire? Mkwiyo wanu ufukiranji pa nkhosa za kubusa kwanu?


Yehova, mudzakwiya nthawi zonse kufikira liti? Nidzatentha nsanje yanu ngati moto?


Ndipo ngakhale Ambuye adzakupatsani inu chakudya cha nsautso, ndi madzi a chipsinjo, koma aphunzitsi ako sadzabisikanso, koma maso ako adzaona aphunzitsi ako;


Mwadzikuta ndi mkwiyo ndi kutilondola, mwatipha osachitira chisoni.


Mwadzikuta ndi mtambo kuti pemphero lathu lisapyolemo.