Yehova, musandichititse manyazi; pakuti ndafuulira kwa Inu, oipa achite manyazi, atonthole m'manda.
Masalimo 80:4 - Buku Lopatulika Yehova, Mulungu wa makamu, mudzakwiyira pemphero la anthu anu kufikira liti? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova, Mulungu wa makamu, mudzakwiyira pemphero la anthu anu kufikira liti? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, mudzakwiyira mapemphero a anthu anu mpaka liti? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu Mulungu Wamphamvuzonse, mpaka liti mkwiyo wanu udzanyeka kutsutsana ndi mapemphero a anthu anu? |
Yehova, musandichititse manyazi; pakuti ndafuulira kwa Inu, oipa achite manyazi, atonthole m'manda.
Mwapatsa chimwemwe mumtima mwanga, chakuposa chao m'nyengo yakuchuluka dzinthu zao ndi vinyo wao.
Ndinu Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele. Ukani kukazonda amitundu onse, musachitire chifundo mmodzi yense wakuchita zopanda pake monyenga.
Ndipo tsopano, Mulungu wathu, mumvere pemphero la mtumiki wanu, ndi mapembedzero ake, nimuwalitse nkhope yanu pamalo anu opatulika amene ali opasuka, chifukwa cha Ambuye.
Yehova sadzamkhululukira, koma pamenepo mkwiyo wa Yehova ndi nsanje yake zidzamfukira munthuyo; ndipo temberero lonse lolembedwa m'buku ili lidzamkhalira; ndipo Yehova adzafafaniza dzina lake pansi pa thambo.