Ndimvereni Yehova, ndimvereni, kuti anthu awa adziwe kuti Inu Yehova ndinu Mulungu, ndi kuti Inu mwabwezanso mitima yao.
Masalimo 80:3 - Buku Lopatulika Mutibweze, Mulungu; nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mutibweze, Mulungu; nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Mulungu, tibwezereni mwakale, mutiwonetse nkhope yanu yokondwa, ndipo ife tidzapulumuka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tibwezereni mwakale Inu Mulungu; nkhope yanu itiwalire kuti tipulumutsidwe. |
Ndimvereni Yehova, ndimvereni, kuti anthu awa adziwe kuti Inu Yehova ndinu Mulungu, ndi kuti Inu mwabwezanso mitima yao.
Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani? Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.
Mbusa wa Israele, tcherani khutu; inu wakutsogolera Yosefe ngati nkhosa; inu wokhala pa akerubi, walitsani.
Mutitembenuzire kwa Inu, Yehova, ndipo tidzatembenuzidwadi, mukonzenso masiku athu ngati kale lija.