Ndipo ansembe analonga likasa la chipangano cha Yehova kumalo kwake, ku chipinda chamkati, ku malo opatulika kwambiri, munsi mwa mapiko a akerubi.
Masalimo 80:2 - Buku Lopatulika Utsani chamuna chanu pamaso pa Efuremu ndi Benjamini ndi Manase, ndipo mutidzere kutipulumutsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Utsani chamuna chanu pamaso pa Efuremu ndi Benjamini ndi Manase, ndipo mutidzere kutipulumutsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa dziwonetseni kwa mafuko a Efuremu ndi Benjamini ndi Manase. Onetsani mphamvu zanu, ndipo mubwere kudzatipulumutsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kwa Efereimu, Benjamini ndi Manase. Utsani mphamvu yanu; bwerani ndi kutipulumutsa. |
Ndipo ansembe analonga likasa la chipangano cha Yehova kumalo kwake, ku chipinda chamkati, ku malo opatulika kwambiri, munsi mwa mapiko a akerubi.
Napemphera Hezekiya pamaso pa Yehova, nati, Yehova Mulungu wa Israele wakukhala pakati pa akerubi, Inu ndinu Mulungu mwini wake, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi; munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Galamukani, ndipo khalani maso kundiweruzira mlandu wanga, Mulungu wanga ndi Ambuye wanga.
Koma Iye pokhala ngwa chifundo, anakhululukira choipa, osawaononga; nabweza mkwiyo wake kawirikawiri, sanautse ukali wake wonse.
Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere; Iye akhala pakati pa akerubi; dziko lapansi ligwedezeke.
Ndipo pomwepo ndidzakomana ndi iwe, ndi kulankhula ndi iwe, ndili pamwamba pa chotetezerapo, pakati pa akerubi awiriwo okhala pa likasa la mboni, zonse zimene ndidzakuuza za ana a Israele.
Ndipo adzanena tsiku limenelo, Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tamlindirira Iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tamlindirira Iye, tidzakondwa ndi kusekerera m'chipulumutso chake.
Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.
Chifukwa chake anatumiza ku Silo kuti akatenge kumeneko likasalo la chipangano la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa akerubi; ndipo ana awiriwo a Eli, Hofeni ndi Finehasi anali komweko ndi likasa la chipangano la Mulungu.