Ezara amene anakwera kuchokera ku Babiloni, ndiye mlembi waluntha m'chilamulo cha Mose, chimene Yehova Mulungu wa Israele adachipereka; ndipo mfumu inampatsa chopempha iye chonse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wake.
Masalimo 80:18 - Buku Lopatulika Potero sitidzabwerera m'mbuyo kukusiyani; titsitsimutseni, ndipo tidzaitanira dzina lanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Potero sitidzabwerera m'mbuyo kukusiyani; titsitsimutseni, ndipo tidzaitanira dzina lanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono sitidzakusiyaninso, tipatseni moyo, ndipo tidzatama dzina lanu mopemba. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ife sitidzatembenukira kumbali kuchoka kwa Inu; titsitsimutseni ndipo tidzayitana pa dzina lanu. |
Ezara amene anakwera kuchokera ku Babiloni, ndiye mlembi waluntha m'chilamulo cha Mose, chimene Yehova Mulungu wa Israele adachipereka; ndipo mfumu inampatsa chopempha iye chonse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wake.
Pakuti tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndilo chiyambi cha ulendo wokwera kuchokera ku Babiloni, ndi tsiku loyamba la mwezi wachisanu anafika ku Yerusalemu, monga linamkhalira dzanja lokoma la Mulungu wake.
Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa, mudzatipatsanso moyo, ndi kutitenganso munsi mwa dziko.
Potero ife anthu anu ndi nkhosa zapabusa panu tidzakuyamikani kosatha; tidzafotokozera chilemekezo chanu ku mibadwomibadwo.
Undikoke; tikuthamangire; mfumu yandilowetsa m'zipinda zake: Tidzasangalala ndi kukondwera ndi iwe. Tidzatchula chikondi chako koposa vinyo: Akukonda molungama.