Ndipo Yehova anakaniza mbumba yonse ya Israele, nawazunza, nawapereka m'dzanja la ofunkha, mpaka anawataya pamaso pake.
Masalimo 80:13 - Buku Lopatulika Nguluwe zochokera kuthengo ziukumba, ndi nyama za kuchidikha ziudya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nguluwe zochokera kuthengo ziukumba, ndi nyama za kuchidikha ziudya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nguluŵe zam'nkhalango zimauwononga, ndipo zonse zoyenda m'thengo zimaudya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nguluwe zochokera mʼnkhalango zikuwononga ndipo zirombo za mthengo zimawudya. |
Ndipo Yehova anakaniza mbumba yonse ya Israele, nawazunza, nawapereka m'dzanja la ofunkha, mpaka anawataya pamaso pake.
Ndipo tsopano ndidzakuuzani chimene nditi ndichite ndi munda wanga wampesa; ndidzachotsapo tchinga lake, ndipo zidzadyedwa; ndidzagumula linga lake ndipo zidzapondedwa pansi;
Mkango wakwera kutuluka m'nkhalango mwake, ndipo waononga amitundu ali panjira, watuluka m'mbuto mwake kuti achititse dziko lako bwinja, kuti mizinda yako ipasuke mulibenso wokhalamo.
Chifukwa chake mkango wotuluka m'nkhalango udzawapha, ndi mmbulu wa madzulo udzawafunkha, nyalugwe adzakhalira m'mizinda mwao, onse amene atulukamo adzamwetulidwa; pakuti zolakwa zili zambiri, ndi mabwerero ao achuluka.
Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wandidya ine, wandiphwanya ine, wandiyesa ine ngati mbiya yopanda kanthu, wandimeza ngati ng'ona, wadzaza m'kamwa mwake ndi zotsekemera zanga, wanditaya ine.
Pamenepo anaboola mzinda, ndipo anathawa amuna onse a nkhondo, natuluka m'mzinda usiku panjira ya kuchipata cha pakati pa makoma awiri, imene inali pamunda wa mfumu; Ababiloni alikumenyana ndi mzinda pozungulira pake, ndipo anapita njira ya kuchidikha.
Koma unazulidwa mwaukali, unaponyedwa pansi ndi mphepo ya kum'mawa, inaumitsa zipatso zake, ndodo zake zolimba zinathyoka ndi kuuma, moto unazitha.
Zikopa za amphamvu ake zasanduka zofiira, ngwazi zivala mlangali; magaleta anyezimira ndi chitsulo tsiku la kukonzera kwake, ndi mikondo itinthidwa.