Tsiku lomwelo Yehova anapangana chipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pamtsinje wa ku Ejipito kufikira pamtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate:
Masalimo 80:11 - Buku Lopatulika Unatambalitsa mphanda zake mpaka kunyanja, ndi mitsitsi yake kufikira ku Mtsinje. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Unatambalitsa mphanda zake mpaka kunyanja, ndi mitsitsi yake kufikira ku Mtsinje. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthambizo zidafika mpaka ku nyanja yaikulu yakuzambwe, ndipo mphukira zake mpaka ku mtsinje waukulu wakuvuma. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Unatambalitsa nthambi zake mpaka ku nyanja, mphukira zake mpaka ku mtsinje. |
Tsiku lomwelo Yehova anapangana chipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pamtsinje wa ku Ejipito kufikira pamtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate:
Ndipo Solomoni analamulira maiko onse, kuyambira ku Yufurate kufikira ku dziko la Afilisti ndi ku malire a Ejipito; anthu anabwera nayo mitulo namtumikira Solomoni masiku onse a moyo wake.
Pakuti analamulira dziko lonse lili tsidya lino la Yufurate, kuyambira ku Tifisa kufikira ku Gaza, inde mafumu onse a ku tsidya lino la Yufurate; nakhala ndi mtendere kozungulira konseko.
Ndipo Davide anakantha Hadadezere mfumu ya Zoba ku Hamati, pomuka iye kukhazikitsa ulamuliro wake ku mtsinje wa Yufurate.
Ndipo adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuchokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi.
Ndipo ndidzalemba malire ako kuyambira ku Nyanja Yofiira, kufikira ku nyanja ya Afilisti, ndi kuyambira kuchipululu kufikira ku Nyanja; popeza ndidzapereka okhala m'dzikolo m'dzanja lako, ndipo uziwaingitsa pamaso pako.