Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pang'ombe, ndi padziko lonse lapansi, ndi pazokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi.
Masalimo 8:7 - Buku Lopatulika nkhosa ndi ng'ombe, zonsezo, ndi nyama zakuthengo zomwe; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nkhosa ndi ng'ombe, zonsezo, ndi nyama za kuthengo zomwe; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa nkhosa, ng'ombe ndi nyama zakuthengo, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe pamodzi ndi nyama zakuthengo, |
Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pang'ombe, ndi padziko lonse lapansi, ndi pazokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi.
Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.
Adamu ndipo anazitcha maina zinyama zonse, ndi mbalame za m'mlengalenga ndi zamoyo zonse za m'thengo: koma kwa Adamu sanapezeke womthangatira iye.