Masalimo 79:5 - Buku Lopatulika Yehova, mudzakwiya nthawi zonse kufikira liti? Nidzatentha nsanje yanu ngati moto? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova, mudzakwiya nthawi zonse kufikira liti? Nidzatentha nsanje yanu ngati moto? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mpaka liti, Inu Chauta? Kodi mudzakhalabe wokwiya mpaka muyaya? Kodi nsanje yanu idzayakabe ngati moto? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mpaka liti Inu Yehova? Kodi mudzakwiya mpaka muyaya? Kodi mpaka liti nsanje yanu idzayaka ngati moto? |
Bwererani Yehova, landitsani moyo wanga; ndipulumutseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu.
Mudzabisala kosatha kufikira liti, Yehova; ndi kuzaza kwanu kudzatentha ngati moto kufikira liti?
Musakwiye kopambana, Yehova, musakumbukire zoipa nthawi zonse; taonani, yang'anani ife, tikupembedzani Inu, ife tonse tili anthu anu.
chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Zoonadi pa nsanje yanga yodya nayo moto ndinanena motsutsana nao amitundu otsala, ndi Edomu yense, amene anadzipatsira dziko langa likhale cholowa chao ndi chimwemwe cha mtima wonse, ndi mtima wopeputsa, kuti alande zake zonse zikhale zofunkha.
Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.
Ngakhale siliva wao, ngakhale golide wao sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova; koma dziko lonse lidzatha ndi moto wa nsanje yake; pakuti adzachita chakutsiriza, mofulumira, onse okhala m'dziko.
Chifukwa chake, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira Ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima Ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga.
Ndipo mthenga wa Yehova anayankha nati, Yehova wa makamu, mudzakhala mpaka liti osachitira chifundo Yerusalemu, ndi mizinda ya Yuda, imene munakwiya nayo zaka izi makumi asanu ndi awiri?
Yehova sadzamkhululukira, koma pamenepo mkwiyo wa Yehova ndi nsanje yake zidzamfukira munthuyo; ndipo temberero lonse lolembedwa m'buku ili lidzamkhalira; ndipo Yehova adzafafaniza dzina lake pansi pa thambo.
Pakuti wayaka moto mu mkwiyo wanga, utentha kumanda kunsi ukutha dziko lapansi ndi zipatso zake, nuyatsa maziko a mapiri.
ndipo anafuula ndi mau aakulu, ndi kunena, Kufikira liti, Mfumu yoyera ndi yoona, muleka kuweruza ndi kubwezera chilango chifukwa cha mwazi wathu, pa iwo akukhala padziko?